Mafuta agalimoto komanso magetsi takweza – MERA


Wolemba: Misheck Silat Phiri - Pali chiyembekezo kuti miyoyo ya amalawi ikhala ikupitilirabe kuwawa kutsatila kukwezedwa kwa mitengo ya mafuta agalimoto antundu wa petulo, dizilo komaso parafini, izi zikutanthauza kuti mitengo ya katundu ndi yamayendewe nayo ikwelanso.


Bungwe lomwe limalamulira kayendetsedwe ka ntchito za mafuta komanso magetsi ya Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) yadzidzimutsa anthu italengeza za kukwera kwa mitengo ku usiku wapa 9 November 2023 kudzera muchikalata chomwe chasayidwaa ndi nkhala pa mpando board ya bugweli a Reckford Kampanje.

Kukwera mitengo kwa mafutawa komanso magetsi kwadza patangodutsa tsiku limodzi pomwe banki yayikulu mdziko muno ya Reserve Bank italengeza kuti yagwetsa mphamvu ya ndalama ya kwacha makwacha 44 pa 100 kwacha iliyonse.

Koma ngakhare mitengo ya mafuta ndi magetsi yakwera, unduna wa zamalonda kudzera muchikalata chomwe atulutsa, wachenjeza ochita malonda kuti asatengerepo mwayi nkukweza mitengo ya katundu yemwe iwo akugulitsa mopyolera muyezo. Chikalatachi chati yemwe apezeke akuchita izi alandira chilango.

Kuyambira lero, Petulo azigulitsidwa pa mtengo wa Mk2,530 kuchoka pa Mk1,746, Dizilo ali pa Mk2,734 kuchoka pa Mk1,220 ndipo Parafini wafika pa Mk1,910 kuchoka pa Mk1261 pa lita.

Ndipo mtengo wogulira magetsi watsopano ndi Mk173.70Kwh kuchoka pa Mk123.26kwh.


(0) Comments


Leave a Comment