Gulu la zachifundo la Happiness lathandiza ovutika ku Lilongwe


Wolemba: MISHEK SILAT PHIRI - LILONGWE Gulu la zachifundo la ogwira ntchito ku kampani ya Export Trading Group (ETG) lotchedwa Happiness Group lapereka katundu osiyana-siyana kwamayi ovutika omwe amakhala mdera la Kaliyeka ku Area 23 mumzinda wa Lilongwe.


Polankhula pamwambo wopereka katunduyi, m’modzi mwa mamembala agululi a Fellix Kazambala anati anachiwona chinthu chabwino kuthandiza anthuwa omwe makamaka akuvutika ndi njala.

"Ngati gulu la zachifundo tinachiwona chanzeru kuti tibwere kuno kwa Kaliyeka kuzathandiza anzathuwa ndi kangachepe komwe tapeza posonkherana," anafotokoza motero bambo Kazambala.

Katundu yemwe anthuwa alandira ndi monga Soya Pieces komanso mpunga zomwe, malingana ndi a Kazambala ndizandalama zokwana MK320,000.00.

M'mawu awo a mfumu akudelari a Kanyamula ayamikira gulu lazachifundoli kamba kothandiza anthu ake chifukwa choti anthu ambiri mderali akuvutika ndinjala.

Aka sikoyamba gululi kupereka thandizo lotere mderali kamba koti m’mbuyomu linagawanso zofunda (blankets).

Gulu la zachifundo la Happiness lakhala likuthandiza anthu ovutika m’madera osiyana-siyana popereka katundu monga zakudya, zofunda, mwazina; ndipo posachedwapa gululi lidaperekanso thandizo lakatundu osiyana-siyana ku sukulu za ophunzira aulumali osawona ndi osamva za Malingunde - Lilongwe ndi Chilanga - Kasungu.

Gululi likupempha anthu akufuna kwabwino kuti agwirane nalo manja pothandiza anthu ovutika omwe akupezeka m’madera ambiri mdziko muno.

Izi zikudza pomwe mtsogoleri wadziko lino Lazarus Chakwera walengeza kuti m’maboma 23 a mdziko muno muli njala.


(0) Comments


Leave a Comment